"chifukwa chimenechi yense amene akamva mawu anga amenewa, ndikuwachita, ndidzamfaninzira Iye ndi munthu amene anamanga nyumba yache pathathwe; ndipo anagwa mvula, nidzala mitsinje ndipo zinaomba mphepo, zinagunda pa nyumba; koma siinagwe", (Mathayo 7:24 na 25).

David ndi Veronique Holland ndi atumiki ozonzedwa amene amakhala ku France. Masophenya awo ndi ndi kuphunzitsa ndi kulalikira mawu a Mulungu popanda kuwiringula ku mafuko momveka bwino ndicholinga chakuti anthu angakakhale chomwe mawu akunena pamoyo wawo. Amachita zimenezi kupyolera kumaphunziro a Baibulo otumiza, mu chingerenzi ndi chi falansa. Palinso ziphunzitso zina zomwe zinayikidwa pamakina a entaneti ndipo maphunzirowa atathauziridwa ku zilakhulo zina zambiri za dziko lapansi. Komanso pali mabukhu ndi ma CD zomwe ziri ndi maphunziro akuti afikire anthu onse.