David Holland

Yesu anawachiritsa odwala molimba mtima ndipo anamuvera iye mozipeleka. Chomwe ndikufuna kuyang’ana pamodzi ndi iwe muchiphunzitso chinechi ndi momwe amawalimbikisira anthu mtima kuti achiritsidwa ku khungu lawo, kusamva ndi matenda amitundumitundu.

Ophunzira wake Mateyu, amane anali okhometsa misonkho asanakhale osatira wa Yesu, amadziwa malemba achipangano cha tsopano. Nthawi zambiri muuthenga wake wabwino, amalakhula zamomwe Yesu anakwanilitsira mauneneri omwe anachitika zaka zochuluka zapitazo.

Chimodzi mwa zitsanzo chake ndi kukwaniritsidwa kwa kubadwa kwa Yesu pa Yesaya 7:14. Koma lero phunziro lathu liri pa machiritso.

Panene madzuro anakwana, anabweretsa ambiri ogwidwa ndi mizimu ya ziwanda ndipo anayitulutsa mizimu yoyipa ndi mawu ndikuchilitsa onse. Kuti mawu a Yesaya mneneri akwanilitsidwe,” (Yesaya 53:4)

Choncho tiyeni tione chomwe Yesaya analemba zaka 800 Yesu asanabadwe. Polakhula za mtumiki obvutidwa anati: “Koma Iye analasidwa chifukwa chazolakwa zathu, natundudzidwa chifukwa cha mphulupulu zathu; chilungamo chititengera ife mtendere chinamugwera Iye; ndipo ndi mikwigwirima yake ife tinachiritsidwa”. (Yesaya 53:5).

Yesaya anali m’neneri. Anali ndi mphatso yauzimu yakutha kuona zithu zomwe zitazachitike m’songolo. Anawoneratu zikwapu zomwe atsilikali a Pilato atazamukwapulenazo Yesu asanapachikidwe. Inali nthawi imeneyi yomwe Yesu “ ananyamula matenda athu ndikunyamula madwale athu.,” koma Yeseya anawona zikuchitika ndipo monga mwa mawu auneneri Yesu anali ndi ulamuliro okwanilitsa mawu ndikuchilitsa odwala angakhale malipiro ake anali asanapelekedwe. Ukhonza kunena kuti anachilitsatu matenda!

Chifukwa chakuti Yesaya analakhula: “Tinachilitsidwa,” Yesu akanatha kuchita, monga momwe Yesaya ananenera, Kunatheka kubadwa kuchokera kwa namwari.

Mmenemu ndi momwe Mulungu amagwirira ntchito; “Palibe chomwe Mulungu angachite”(Amosi 3:7)

Yesaya anaona Yesu akukwapulidwa zisanachitike. Mtumwi Peturo analipo ndipo anaona ndi maso ake atayima patali(Luka 22:54). Anawonerera zobvetsa chitsoni ndipo analemba kuti: “ Ndimikwigwirima yake tinachiritsidwa,”(1 Pet. 2:24)

Peturo amayang’ana mbuyo ndikunena kuti machiritso anakwaniritsidwa. Yesaya anayang’ana mtsongoro ndikulakhula ngati zachitika kale.

Kodi zimenezi zikutathauza chiyani kwa Ife? Choyamba tikuyenera kulingalira kuti mtengo wake wa matenda unalipilidwa kale. Choncho sitichitanso kudandaulula kuti tichiritsidwe. Anatichiritira kale chimenechi, choncho tikhonza kukhala ndikulimbika mtima mu msembe yomwe inapelekedwa kale(Ahebri 10:14)

Mu a Aroma 6, Mtumwi Paulo analemba kuti ndi kubwerenzanso choonadi chakuti munthu wathu wakale anapachikidewa ndi Khristu(1-10). Kenaka mu vesi 11 akutiuza kuti “ muziyese nokha akufa kuuchimo.” Mu njira ina muzione kuti zilichimwecho!

Angakhale titakhala ndi zizindikiro za matenda, muzilingalire koma muzione nokha ochiritsidwa. Khulupilira kuti wachira. Kuti zimenezi zikhale choncho muzifunse nokha mafutso atatu awa.

  1. kidi ndikuopa kufa? Pokhapokha titathana ndi matha akufa, tizakhalabe akapolo amatha a imfa(AHeb.2:15).
  2. Ngati Yesu angaime pamanso panu ndikukumfutsani kuti: “Ukuganiza kuti ndinalephera kupeleka nsembe ya matenda ako?”Unganene chiyani? Ndikukhulupilira kuti ungamvomereze kuti palibe myhenda yomwe anayiyiwala osaipelekera nsembe. Anapeleka nsembe ya zonse.
  3. Yesu anali pompo mmene nzikachitika, kulandira zikwapu zopweteka, ukuganiza kuti analipira mtengo onse wa nthenda zako zonse?

Ngati ukuchita mantha kufa, ndiye kuti sungagonjetse matenda. Ongonjetsa amakhulupilira mwanzi wa mwana wa nkhosa, amachitira umboni za zimenezi ndipo samakonda moyo wawu angakhale imfa.(Chibvumbulutso 12:11).

A.W.Tozer anatathauzira kuti chikhulupiriro choona ndi kuziyika wekha pamalo pakuti ngati Mulungu angakusiye ndiye kuti umfa.

Chikhulupiliro chabonza anachitathauzira kuti pamene timakhala ndi maganizo obwerera m’buyo, kuti nanga ngati Mulungu salowerera. Mwachitsanzo, kukhulupilira kuti tachilitsidwa koma kumasungabe nambala ya Dokotala, kapena yakuchipatala. Kumeneku ndikukhala ndi maganizo ogawikana ndipo palibe chomwe titazalandire kuchokera kwa Mulungu (Yakobo 1:4-8).

Ngati mukudwala, khulupilirani Mulungu ndikukhulupirita mawu ake. Ndipakhulupirira Mulungu amene samasitha pamene sitimangolandira machilitso okha komanso tinganene molimba mtima kuti amatithandiza muzosowa zathu zonse.